tatewachikondi.com

Takulandirani ku Tate wa Chikondi! Ife ndife okondwa kwambiri poti mwaima pano. Pa webusaitii ife tikugawana ndi inu uthenga wabwino kwambiri okhuzana ndi khalidwe la Mulungu wathu wachifundo, okonda – ndipo pamene mukuwerenga, inu mudzamvetsa chifukwa chimene ife tiri okhutira kwambiri kuti Iye alidi Mulungu wa chikondi. Pali zinthu zambirizi anthu samvetsa za khalidwe la Mulungu – ngakhale Akristu odzipereka kwambiri!

Satana wapanga zotheka (ndipo nthawi zambiri kupambana) kuwapanga anthu kukhulupirira kuti Mulungu ali ndi makhalidwe ake (a Satana) – mkwiyo, kubwezera, ndi kupha – m’malo mwa makhalidwe a Mulungu Mwini watiuza ife m’Baibulo: chikondi, kuleza ndi kupirira.

“Nanga bwanji za nkhani m’Chipangano Chakale m’mene Mulungu akupha ndi kulamulira kupha?”inu mukhoza kufunsa. Ife tafunsanso mafunso omwewo – chifukwa Mulungu otere sagwirizana ndi Mulungu wabvumbulutsidwa mwa Yesu m’Chipangano Chatsopano – ndipo chidziwitsochi chotsutsana ndichosokoneza kwa aliyense amene amayesa kumvetsetsa chifukwa chake Mulungu ndi Mulungu wa chikondi.

Zimene mudzapeza mu webusatii ndi zotsatira zakufufuza kwa zaka khumi zisanu ndi chimodzi kuyesa kuphunzira za Mulungu ndim’mene Iye aliridi. Buku liri lonse likuonetsera kuphunzira Baibulo mosamala ndi mwakuya pa mitu tiri nayo pano. Ife tikukhulupirira kuti likhala dalitso kwambiri kwa inu monganso lakhalira kwa ife. Kuli ufulu ochuluka ndi chimwemwe m’kudziwa, ndi otsimikizika, kuti Mulungu moona ndi Mulungu wa chikondi, ndikuti ife ndife okondedwa mwakuya ndi Iye.

Ngati kali koyamba kuona webusatii, tiloleni tikuunikireni m’mene mungayambire kuwerengera mwa ndondomeko yake:

      Nkhondo za Kudziwika: M’dziko m’mene mamiliyoni a anthu ambiri akuvutika chifukwa cha zotsatira za kuzimva kuti ndiachabechabe / osayenera, m’mene zikwizikwi ali ofoka poyetsetse kukhalabe akuchita bwino kuti aziwerengedwa, ndi m’mene zikwizikwi zambiri zingololera kukhala ndi nkhawa chifukwa cha malingaliro awo a uchabechabe, Mulungu akufuna kutipatsa ife chitsimikizo kuti ife ndife okondedwa ndi a mtengo wapatali. Bukuli likufotokoza za “nkhondo zathu za kudziwika”- kuchokera ku maganizo a uchabechabe ndi osakhala okwanira, kunka kukulandiridwa mwa mtendere wa kuyenera kwenikweni – kusintha kwa moyo kotsimikizika – kopatsidwa kwa ife ndi Mulungu kudzera kwa Mwana Wake.

     Machitidwe a Mulungu wathu Waulemu: Mau oyamba abwino okongola a phunziro la khalidwe la Mulungu. Mulungu sakakamiza mwamphamvu kapena mwachiwawa. Iye ndi waulemu ndi wokoma mtima. Taonani umboni wa m’Baibulo za Mulungu okonda moonadi.

     Nzeru ya Mulungu: Pachiyambi Mulungu anapanga chirengedwe m’njira yapaderadera kuonetsetsa kuti pakhale ubwenzi weniweni pa ana Ake olengedwa. Phunzirani nzeru ya Mulungu yakale m’mene Iye anayamba chirengedwe ndi chifukwa chake.

     Mtanda Ofufuzidwa ndi Mtanda Okumananawo: Chifukwa chani Mtanda unafunika ndipo ndindani anaufuna? Mtanda unasintha mitima ya anthu bwanji ndikuwatsogolera ku chipulumutso? Kodi kachitidwe ka chiwawa kangathe bwanji kutsogolera ku moyo wa mtendere?

     Chikondi Chenicheni: Yesu anamuuza ophunzira wake Filipo kuti Atate Akumwamba ali monga Iye m’Chikhalidwe. Bukuli likuonetsa m’mene zonena Kristu nzolondola m’kuwala kwa chiwawa chonse chimaoneka m’Malemba kwenikweni m’Chipangano Chakale. Ichi nchotsatira changwiro cha Machitidwe a Mulungu wathu Waulemu.

     Wotonthoza: Dziko mwamsanga likufuna ubwenzi weniweni koma dziko likukopeka ku kugonana, zolaula, ndi zachisembwere kupeza kukwanitsidwa koma kupeza zotsutsana ku ubwenzi woona. Kodi cholinga cha Mulungu pa ubwenzi wa mwamuna ndi mkazi ndi chani? Chifukwa chani amuna ambiri ali ndi chibaba cha zolaula? Ndindani ali ndi gwero lenileni la chitonthozo chathu ndipo tipange bwanji kuti tipeze ubwenzi woona m’maubale athu?

     Chitsanzo cha Moyo wa Umulungu: Ubale wa Mulungu Atate ndi Mwana Wake, Yesu Kristu, monga zafotokozedwa mu 1 Akorinto 8:6, ndi chinsinsi chomvetsetsa choonadi chofunikira kwambiri cha Baibulo. Ndichosavuta komabe “chilinganizo” chofunika kwambiri osati kokha kutsegula ziganizo za Baibulo, komanso kumvetsetsa maubale ena m’moyo.