tatewachikondi.com
Wolemba Adrian Ebens
Losindikizidwa Seputombala 21, 2020
Zokopera 958

Yemwe ali ndi Mwana mwa iye alinso ndi moyo. Kodi izi zili chomwechi bwanji? Mwa Mwana wa Mulungu muli mtima moyera omwe uli womvera Atate ake. Nthawi zonse amapanga zosangalatsa Atate ake. Komanso ali ndi mdalitso wa Atate ake ndi kukhunzika ndichikondi. Mtima wa Mwana ndiwokhazikika m'chikondi cha Atate ake.

Ndi nzeru ya Atate kugawana Mzimu wa chikondi cha Mwana wake wokondedwa ku chilengedwe chonse; kukoma, kudekha ndi Mzimu omvera wokonda malamuro a Atate ake. Khristu ndi nzeru ya Mulungu ndi chitetezo chachikondi mu ufumu wa ubale.

Mzimu wozichepetsawu umasefukira kuchokera ku mpando wa Mulungu kutsikira kupyorera mtengo wa moyo. Satana anakana Mwana wa Mulungu ndi Mzimu wake wozichepetsa. Mzimu wake wowukira unali pankhondo ndi Mzimu ozichepetsa, omvera, wabwino wa Mwana wa Mulungu. Mzimu owukirawu udasefukira mwa mitundu ya anthu. Mu nsembe ya Yesu Khristu tikupasidwanso Mzimu wozichepetsawo. Chinsinsi chokhala ndi Mzimuwu ndikudziwa za momwe Atate ndi Mwana  alili- uwu ndi moyo wosatha kumuziwa Atate ndi Mwana wake ndi kumwa madzi a moyo a kasupe wochokera ku mpando wa Mulungu ndi mwana wa Nkhosa.