Mabuku
Chikondi Choyambirira
Tili ndi chiyembekezo kuti titha kusunthidwa m’mitima yathu kubwerera ku chikondi choyambirira.
Chitsanzo Chaumulungu Cha Moyo
Zitsanzo za dziko lonse za moyo zonse zimatizungulira ife. Zonse zimachokera ku Chitsanzo Chaumulungu choyambirira chotsika kuchokera kwa Atate, kudzera mwa Mwana ndipo chimapezeka pa mulingo uliwonse wa moyo.
Machitidwe a Mulungu Wathu Wofatsa
Machitidwe a Mulungu Wathu Wofatsa akupereka umboni wotsimikizira kuchokera m’Baibulo woneneza Mulungu kuti Iye ndi wosasamala, woweluza, wolamulira, wokondera, wokwiya, kapena wachiwawa. Bukuli likuwonetsa kuti Baibulo lonse, momveka bwino, limagwirizana ndi mawu womveka bwino akuti: “Mulungu ndiye chikondi” (1 Yohane 4:8).
Mtanda Ofufudzidwa ndi Mtanda Okumananawo
Nchifukwa chiyani Mtanda unkafunika ndipo ndani anaufuna?
Nchifukwa chiyani Mtanda unali wofunikira pa chipulumutso chathu?
Kodi mkwiyo wa Mulungu unakwaniritsidwa ndi imfa ya Mwana Wake?
Kodi chilungamo cha Mulungu ndi chiyani ndipo ndi chosiyana ndi chilungamo chathu?
Chifukwa chiyani Yesu adadzifanizira ndi njoka ya mkuwa pa mtengo?
Kodi malo opatulika achi Israeleakutiuza chiyani za Mtanda?
Nkhondo za Kudziwika
Nkhondo za Kudziwika ndi ulendo wa kuzipeza wekha. Uku ndi kuyitanira ku kuphunzira phindu lanu mu nkhani za ubale.
Nzeru ya Mulungu
Yemwe ali ndi Mwana mwa iye alinso ndi moyo. Kodi izi zili chomwechi bwanji? Mwa Mwana wa Mulungu muli mtima moyera omwe uli womvera Atate ake. Nthawi zonse amapanga zosangalatsa Atate ake. Komanso ali ndi mdalitso wa Atate ake ndi kukhunzika ndichikondi. Mtima wa Mwana ndiwokhazikika m'chikondi cha Atate ake.
Ndi nzeru ya Atate kugawana Mzimu wa chikondi cha Mwana wake wokondedwa ku chilengedwe chonse; kukoma, kudekha ndi Mzimu omvera wokonda malamuro a Atate ake. Khristu ndi nzeru ya Mulungu ndi chitetezo chachikondi mu ufumu wa ubale.
Mzimu wozichepetsawu umasefukira kuchokera ku mpando wa Mulungu kutsikira kupyorera mtengo wa moyo. Satana anakana Mwana wa Mulungu ndi Mzimu wake wozichepetsa. Mzimu wake wowukira unali pankhondo ndi Mzimu ozichepetsa, omvera, wabwino wa Mwana wa Mulungu. Mzimu owukirawu udasefukira mwa mitundu ya anthu. Mu nsembe ya Yesu Khristu tikupasidwanso Mzimu wozichepetsawo. Chinsinsi chokhala ndi Mzimuwu ndikudziwa za momwe Atate ndi Mwana alili- uwu ndi moyo wosatha kumuziwa Atate ndi Mwana wake ndi kumwa madzi a moyo a kasupe wochokera ku mpando wa Mulungu ndi mwana wa Nkhosa.