tatewachikondi.com
Losindikizidwa Epulo 05, 2024
Zokopera 76

Zinenero Zina

Afrikaans English Español Kiswahili

Khristu amatiuza kuti Mawu a Mulungu ndi choonadi.

Koma pali zikhulupiriro zosiyanasiyana, ndipo mwachionekere zonsezo zimachokera m’Baibulo, choncho ife tingadziwe bwanji? Nanga tingadziwe bwanji choonadi pamene tikupeza kuti m’Baibulo muli zinthu zooneka ngati zotsutsana?

Baibulo lenilenilo limatiphunzitsa mmene tingathetsere mavuto wooneka ngati amenewa, mwa malangizo omveka bwino ndi mafanizo. Pamene ife tikutsatira malangizo a m’Malemba onena za mmene tingalandirire Mawu a Mulungu, kenako mmene timawerengera Baibulo zimasintha kwambiri. Paulo akutilangiza kugawa moyenera Mawu a choonadi - tingachite bwanji choncho?

Kuyankha mafunsowa, werengani m’kabukuka maziko a Mfundo Kapena Malamulo Omasulira, amene Baibulo limalengeza.