tatewachikondi.com
Wolemba Adrian Ebens
Losindikizidwa Seputombala 29, 2020
Zokopera 1,027

Nkhondo za Kudziwika ndi ulendo wa kuzipeza wekha. Uku ndi kuyitanira ku kuphunzira phindu lanu mu nkhani  za ubale.

Miyoyo yathu yimavutitsidwa ndi mauthenga ambiri wotiuza ife kuti kupambana kumabwera kuchokera podzitsimikizira ife tokha ndi dziko kuti tiri nazo zotiyenereza, kuti tiri ndi zinthu zoyenera. Ndi dongosolo lotiphunzitsa ife kuzimva a phindu ndi ofunika pamene takwanitsa ndi kuchita kufika pa mlingo wina wake. Zotsatira za dongosololi ziripo ndipo umboni wake siwabwino. Zikwizikwi za anthu amataya mtima ndipo mazanamazana a anthu pa tsiku amachotsa miyoyo yawo chifukwa chokhumudwa.

Ndikukuyitanirani kukuphunzira choonadi cha khalidwe la nkhondo tirimo – nkhondo za kudziwika ya zomwe zimathandauzira phindu ndi kufunika kwathu. Chiopsezo nchachikulu chifukwa ichi ndi moyo kapena imfa. Bukuli liri ndi ulendo wanga ndi mfundo ndinaphunzira pa njirayi. Ufulu ndi chinthu cha chibale koma bukuli likulemba msewu wanga ku ufulu.