tatewachikondi.com

Iye Sangathe Kudzipulumutsa Yekha

506 Kugunda

“‘Iye Sangathe Kudzipulumutsa Yekha’” The Medical Missionary 7, 7.

Wolemba E. J. Wagoner M.D.

Pamene Yesu anapachikidwa pa mtanda, ansembe ndi alembi ndi akulu ananena monyoza, “Iye anapulumutsa ena; Iye sangathe kudzipulumutsa Yekha.” Mateyu 27:42. Ndipo m’mawu amenewa munali chowonadi choposa chimene Ayuda sanachiganizire nkomwe, chowonadi chimene ngakhale otsatira a Yesu samachiyamikira. Aliyense amene angamvetse tanthauzo la mawu akuti, “Iye anapulumutsa ena; Iye sangathe kudzipulumutsa Yekha,” ndipo amene amalola kuwagwiritsa ntchito kwa iyemwini, ali ndi chipulumutso, chifukwa chakuti ali ndi uthenga wabwino wonse.

“Iye anapulumutsa ena.” Ayuda anabvomereza zimenezi, komabe iwo anamupachika Iye. Iye amene cholakwa chake chokha chinali chakuti “anayendayenda nachita zabwino,” anapachikidwa monga wochita zoipa, ndipo Iye sanatambasule dzanja lirironse m’kudzitetezera Yekha, kapena kunena mawu achitonzo kwa om’zunza Ake. “Iye anatsenderezedwa, nazunzidwa, koma Iye sanatsegula pakamwa Pake; Iye wabweretsedwa ngati mwanawankhosa wopita kukaphedwa, ndi ngati mwana wankhosa ali wosalankhula pamaso pa omsenga, motero sanatsegula pakamwa Pake. Yesaya 53:7. Iye anapulumutsa ena, ndipo ngakhale pamene anapachikidwa pa mtanda, “otonzedwa wa anthu, ndi onyozedwa wa anthu,” Iye anasonyeza mphamvu yake ya kupulumutsa, pa mlandu wa mbala wolapayo; koma Iye sanathe kudzipulumutsa Yekha.

Ndipo ichi chinali chinsinsi cha mphamvu Yake yopulumutsa ena. Sikunali kuti sakanatha kudzipulumutsa, osatinso kuti Iye wosadzikonda anadziiwala Yekha, koma Iye sanathe kudzipulumutsa Yekha. Kudzipulumutsa Yekha kukanakhala chiwonongeko cha ena onse; pakuti ngati Iye anakonza kudzipulumutsa Yekha, Iye akanakhala kumwamba, ndikusadziwonetsera Yekha ku chitonzo ndi nkhanza. Koma chinthu choterocho chinali chosatheka; kotero Iye sakanatha kudzipulumutsa Yekha, pakuti kudzipulumutsa Yekha koteroko kukanakhala kudzikonda, ndipo munalibe kudzikonda mwa Iye. Iye sakanathabe kukhala kumwamba ndi kusiya munthu kuti awonongeke. Koma Iye sakanatha kupulumutsa anthu, pamene akudzisunga Yekha mu chitetezo padera pa iwo ndi mavuto awo. Kotero “anadzipereka Yekha chifukwa cha ife.” Tito 2:14.

Kotero tikuona kuti Uthenga Wabwino uli ndi chiyambi ndi ungwiro pakupereka. “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha…” Yohane 3:16. “Mwana wa Munthu sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira,”- osati kudzatumikiridwa, koma kutumikira, - “ndi kupereka moyo Wake dipo la ambiri.” Mateyu 20:28. “Pakuti mudziwa kuti chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti, ngakhale anali wolemera, adakhala wosauka chifukwa cha inu, kuti inu mwa kusauka Kwake mukakhale olemera.” 2 Akorinto 8:9. Iye anali ndi chirichonse, ndipo ife tinalibe kanthu; kotero adasiya zonse, ndipo Iye sanasunge kanthu, kuti ife tikhale nazo zonse.

Momvekera bwino kwambiri zimenezi zafotokozedwa pa Afilipi 2:7, pamene timauzidwa kuti pamene Yesu anali ndi chirichonse, sanachiyese kukhala chinthu chokhumbidwa kuchigwira, “koma anadzikhuthula yekha…” Liwu Lachihelene limene mawuwa anawamasulira limatanthauza “kukhetsa.” M’lingaliro loti Iye anadziwononga Yekha, anadzitaya Yekha, kuti akapulumutse otayika, ndi pachiwopsezo cha chiwonongeko. Iye sanadziganizire Yekha; Iye sanadzitchinjirize ku zowukira zomwe zinamuchitikira Iye; mosasamala kanthu ndithu, mosasamala za Iye mwini, Iye anataika podera nkhawa za ena.

Kudzinyalanyaza kumeneku sikunali kutengeka mtima kwa kanthaŵi, monga momwe munthu wosonkhezeredwa ndi chisonkhezero champhamvu akupulumutsira mnzake ku imfa yomwe inali kum’yandikira potaya moyo wake. M'malo mwake, chinali cholinga chokhazikitsidwa mwadala. Modekha ndi mwadala, kuyang'ana chochitika chonse, ndikuwerengera mtengo wake, anapereka moyo wake, ndiko kuti, anauyika kuchokera kwa Iye, anaupereka ku ntchito yotumikira ena; ndipo pamene ichi chinachitika, nthawi ya imfa koma inali chochitika mu ntchito yaitali ya kupereka komweko. Moyo wake unali woperekedwadi chifukwa cha nkhosa asanabwere padziko lapansi, ndipo pamene anali kuyenda ndi kulankhula ndi kuzunzika mu Yudeya ndi Galileya, monga pamene ndi mpweya Wake ukutha anafuula, “Atate, m’manja mwanu Ine ndipereka Mzimu wanga.”

M’mbiri yonseyi ya kudzipereka yekha nsembe muli phunziro kwa ife. Sitiyenera kungosirira chitsanzo cha kudzipereka, koma kuchitsatira. M’menemo mokha muli chipulumutso. Yesu zikuoneka kuti anadzitaya, inde, zimenezo n’zimene anachitadi, pakuti “anathira moyo wake ku imfa.” (Yesaya 53:12) “anazikhuthula yekha,” anakhetsa dontho lomalizira; “Chifukwa chakenso Mulungu anamkweza Iye, nampatsa dzina lomwe liposa maina onse.” Afilipi 2:9. Kunyozeka kwake kunali kukwezedwa kwake; kudzitaya kwake kunali chipulumutso chake. Ndipo iyo inali njira yokhayo yotheka ya chipulumutso; pakuti, monga tanenera kale, kufunafuna kudzipulumutsa yekha kukanakhala kudzikana, ndiko kuti, kutsimikizira kukhala wabodza ku chikhalidwe chake. Popeza Mulungu ndiye chikondi, wopanda dyera, njira yokhayo imene angatetezere kukhalapo kwake ndiyo kudzipereka.

“Umo tizindikira chikondi, pakuti Iye anapereka moyo wake chifukwa cha ife; ndipo ifenso tiyenera kupereka moyo wathu chifukwa cha abale.” 1 Yohane 3:16. “Abale” amene tiyenera kudzipereka chifukwa cha iwo ndi ana a Adamu, pakuti onse amene ali ana a Adamu ayenera kukhala abale. Ndithudi iwo amene adzipereka okha chifukwa cha abale awo mwa Adamu, mosakayikira adzadzipereka okha kwa abale awo mwa Kristu, amene iyemwini amawerengera ngakhale iwo amene sadziwa dzina la Mulungu monga abale ake, kuti, “Ndidzalalikira dzina lanu kwa abale anga.” Ahebri 2:12. “Ife tiyenera kupereka moyo wathu chifukwa cha abale.” Osalola wina kunena kapena kuganiza kuti, “Moyo wanga ndi malowamba komanso wosafunikira ndipo ndilibe chifukwa choperekera moyo wanga chifukwa cha aliyense; palibe mwayi waukulu wobwera kwa ine." Simukufa pa chochitika china chachikulu, kuti kutaya moyo wa munthu kumaphatikizapo; kutaya kwa moyo kumaphatikizapo m’kusawerengera ife eni, kudziyesa ife tokha monga akufa, kutaya dala moyo wathu kuchoka kwa ife, ndi kuiwala izo zonse m'kulingalira za ena. “Lolani mtima uwu ukhale mwa inu, umene unalinso mwa Khristu Yesu.”

Phunziro, mwachidule, ndi lakuti palibe amene angapulumutsidwe poyesera kuzipulumutsa. Chipulumutso ndi chinthu chachikulu kwambiri chomwe sichingakwaniritsidwe ndi zoyesayesa za anthu. Ngakhale zingawoneke zodabwitsa, tingapulumutsidwe pokhapokha pamene tisiya zoyesayesa zonse zodzipulumutsa tokha, ndi kutaya lingaliro lonse laundekha m’kuyesayesa kupulumutsa ena. Pokhapo ndipamene timalowa mu chifundo chachikulu ndi Khristu, ndi kukhala antchito limodzi ndi Mulungu. Koma kudzitaya kwa ife eni ndiko chipulumutso chathu, pakuti pamene ife tikulingalira tokha za ena, Khristu, amenenso akulingalira yekha za ena, ndi nkhani ndithu kutisamalira ife. “Mulungu anachotsa ukapolo wa Yobu pamene anapempherera mabwenzi ake.” Yobu 42:10.

Kotero n'zotsimikizirika kwa ife kuti tidzamasuka ku nkhawa. Ndikosavuta bwanji kuponya nkhawa zathu zonse pa Iye, pamene tikudziwa kuti amatisamalira ife. Ndipo pamene tadziwa kuti Iye amatisamalira ife, tifuniranji ife kuzidera nkhawa tokha? Chotero timapeza chowonadi chakuti goli la Ambuye nlophweka, ndi katundu wake wopepuka.

Chinthu chimodzinso. Paulo anati: “Ine ndiri wamangawa kwa Ahelene, ndi kwa akunja, kwa anzeru, ndi kwa opusa. Aroma 1:14. Zimene zinali zoona kwa Paulo nzoona zofanana ndi ifeyo. N’chifukwa chiyani anali wamangawa? Yankho ndi lomveka, pamene ife tikayima kamodzi kuganiza; ndi chophweka, kuti Paulo analandira zonse zomwe zinaperekedwa za dziko lapansi. Khristu anapereka moyo wake chifukwa cha dziko lapansi. Iye “analawa imfa m’malo mwa munthu aliyense.” Koma Kristu sanagawanika; moyo uliwonse umatenga zonse zake. “Ndipo kwa yense wa ife chapatsidwa chisomo, monga mwa muyeso wa mphatso ya Kristu.” Aefeso 4:7. Moyo wake ndi kuwala; ndi kuunika kumene kumawalira ine, kumaunika kwa onse kuwala mofanana. Iye ndiye “Dzuwa la chilungamo; koma dzuwa limawalira onse; aliyense amapeza phindu lonse la dzuwa, ndipo palibe amene akanatha kupeza lochuluka, ngakhale akanakhala yekhayo padziko lapansi. Chotero munthu aliyense amalandira moyo wonse wa Khristu, umene waperekedwa ku dziko lapansi. Tsopano zikuwonekeratu kuti ngati ndipeza zonse zomwe zimaperekedwa kudziko lonse lapansi, kuti ndiri ndi mangawa kudziko lapansi; ndi momwemonso kwa munthu aliyense. Kusiyana kokha pakati pa ambiri a ife ndi Mtumwi Paulo ndiko kuti anazindikira kuti kwa iye kunali chidzalo cha Khristu choperekedwa, ndipo analandira ndi kugawira mphatsoyo, pamene ife kawirikawiri timakhutira ndi pang'ono chabe za moyo waumulungu. Ife mwadyera timaganiza kuti titenge zokwanira kuti tigwiritse ntchito ife tokha, ndikuyika gawo lina padera ndi ife, osazindikira kuti tiyenera kukhala nacho chonse; chotero timalephera kuzindikira kuti ndife amangawa. Mulungu atipatse ife tonse kuti tikhale ndi maso a malingaliro athu ounikiridwa ndi Mzimu Woyera, kuti tidziwe chuma cha ulemerero wa cholowa chake mwa oyera mtima, ndipo tisakane gawo la moyo wa Khristu limene kwa munthu wa thupi la nyama amaona losavomerezeka, koma angalole moyo wake wosadzikonda kotheratu kukhala mwa ife, kotero kuti ife, osati ndi milomo yathu yokha, koma mwa kudzipereka kwathu mokondwera chifukwa cha ena, tiperekedi chiyamiko kwa Mulungu chifukwa cha mphatso yake yosaneneka.