Mkhalapakati Mmodzi
Yolembedwa ndi Adrian Ebens mu Uthenga Wabwino Wamuyaya [Everlasting Gospel]
Pali mkhalapakati mmodzi pakati pa Mulungu ndi munthu, ndiye munthu Khristu Yesu. Palibe njira yofikira kwa Atate kupatula kudzera mwa Iye. Kudziwa Khristu - monga Iye ali - kudzasintha iwo amene amamuwona Iye mu chifaniziro chomwecho; muchimaliziro chomwe chimapezeka nthawi zonse mwa Khristu.
Zolemberazi zikukhazikika pa zaka makumi ambiri za maphunziro a Baibulo mkati mwa gulu lapadera mwachikondi lomwe limatchedwa gulu la Atate wa Chikondi. Ife tadziwa chowonadi cha mawu awa kuchokera ku Umboni wa Yesu:
Kwa iwo amene awona chithunzithunzi cha chowonadi chakumwamba, kwa iwo kwafikira kuwala kwina kwa kuunikira, ndiko chenjezo laperekedwa. Chifukwa cha miyoyo yanu musapatuke ndi kukhala osamvera masomphenya akumwamba. Mwina munawonapo kanthu pa chilungamo cha Khristu, koma pali chowonadi chomwe chiyenera kuwonedwa momveka bwino, ndipo ichi chiyenera kuganiziridwa ndi inu kukhala chamtengo wapatali ngati miyala ya mtengo wapatali. Mudzawona chilamulo cha Mulungu ndi kumasulira kwa anthu mosiyana kwambiri ndi zimene munachita m’mbuyomo, pakuti lamulo la Mulungu lidzawonekera kwa inu ngati likuwululira Mulungu wachifundo ndi chilungamo. Chitetezero, chopangidwa ndi nsembe yopambana ya Yesu Kristu, chidzawonedwa kwa inu mukuwala kosiyana kotheratu. The Signs of the Times, November 13, 1893, ndime. 2
Kutsegula tanthauzo la kuyeretsedwa kwa Kachisi ndi mfungulo wa kumalizika kwa utumiki woperekedwa kwa Seventh-day Adventist. Mpingo unayitanidwira pa malo okwezeka mu 1888, koma mwachisoni unakana kuyitanira kumeneko, pomaliza ndikutseka chitseko kotheratu mu 2001.
Kutolera maulusi a gulu la ma Adventist Woyambirira ndikuyika uthenga wa 1888 pa maziko olimba operekedwa kwa ma Adventist Woyambirira, chithunzi chamtengo wapatali chimatuluka chomwe chimasiya moyo mu ulemu wathunthu. Ndani akanaganiza kuti uthenga wabwino ndi wabwino, wabwino kuposa, momwe inu mukuganizira.
Robert Wieland anaima pafupifupi yekha m’chikhulupirirochi, kupereka zinyenyeswazi za mkate kwa mzimu wanjala umene umasankha kukhulupirira kuti Mulungu anatumiza uthenga wamtengo wapatali kwambiri kupyolera mwa atsogoleri Wagoner ndi Jones. Koma chofunika kwambiri ku uthenga umenewu chinali kukhazikitsidwa kwake pa nsanja yolimba ndi yosasunthika m’gulu la Woyambirira ndi Mulungu amene iwo ankalemekeza ndi kumulambira.
Mu zolemberazi ine ndalumikiza zomwe ndapeza ndi mtima wa uthenga wa 1888 ndi maziko ama Adventist opezeka mu Daniel 8:13, 14:
Lemba limene pamwamba pa ena onse linali ponse maziko ndi mzati wapakati wa chikhulupiriro cha ma Adventist linali chilengezo chakuti: “Kufikira masiku zikwi ziwiri mazana atatu; pamenepo kachisi adzayeretsedwa.” Danieli 8:14. Mukangano Waukulu tsamba 409 ndime yoyamba [The Great Controversy, p. 409.1]
Mukuwala kwa mapangano awiri, amene akazindikiridwa moyenerera, nkhani ya Danieli 8 yivumbulutsa chinthu chabwino kwambiri, kuyeretsedwa kwa kachisi ndiko kuchita kwa Mulungu chabe. Dr Desmond Ford anazindikira chowonadi ichi, koma pokhala wopanda maziko a 1888 kapena maziko a Woyambirira sanathe kumaliza uthenga wamtengo wapatali kwambiri, ngakhale ndimamuthokoza chifukwa cha khama lomwe anachita.
Zizindikiro za unsembe wa Melkizedeki zimatikokera ife kumvetsetsa mozama za dongosolo la chipulumutso ndi kutiyitana ife kuti Atate wathu sanafune konse nsembe ndi zopereka, ndi kuti pamene Khristu ananyamula chikho cha vinyo wa mphesa kwenikweni chimaphiphiritsira chisangalalo cha mtima chimene chimadza kwa ife mu Mzimu pamene tiri ndi chitsimikizo chakuti ife tiri ana a amuna ndi a akazi a Mulungu mwa Khristu Yesu. Ndipo ichi ndi chikhalidwe chachikulu cha unkhoswe wa Khristu; utumiki wa moyo; Mzimu wopatsa moyo. Unsembe wamuyaya.
Koma kodi imfa ya Khristu si yofunika? Kugwa kwa anthu kunachititsa anthu kuwona Atate kudzera m’chiweruzo cha Satana. Kuti afike kwa anthu, Khristu anakhala mkhalapakati wathu kuyimira pakati nsembe yimene tinkafuna chifukwa tinali wokhutira ndi bodza la Satana lakuti tchimo liri lonse liyenera kulangidwa.
Koma Khristu amatitsogolera ife kudutsa guwa la mwazi la nsembe lopangidwa ndi mkuwa ndi kulowa mu chihema cha golide cha Kachisi. Chilakolako cha mwazi cha munthu chiyenera kuchepa ndipo mwazi wa Khristu wopatsa moyo kapena Mzimu uyenera kuwonjezeka.
Ndi pemphero langa kuti mumve mawu a Atate wathu mu zolemberazi akukuyitanani kuti mukhale mmodzi wachimwemwe wa zikwi zana mphambu makumi anayi kudza anayi [144,000]. Monga mu Adventist, mudzayenera kugonjetsa zaka zana zopandukira kuwala. Ndi ntchito yovuta koma kwa Mulungu zonse ndi zotheka. Mupeze mwa Khristu Yesu mkhalapakati wathunthu amene angathe kuyeretsa maganizo athu ku chilungamo chabodza, kuvomereza kudziwika kwathu kuwona mwa Khristu ndi kusindikizidwa ndi mwazi wa moyo wa Khristu; Mzimu Wake; kukhala mmodzi wa banja lakumwamba kwamuyaya - m'dzina la mtengo wapatali la Yesu - Ameni.