tatewachikondi.com
Wolemba Adrian Ebens
Losindikizidwa Marichi 22, 2022
Zokopera 383

Khristu anakweza khalidwe la Mulungu, kumpatsa Iye matamando, ndi kumpatsa Iye ulemu, ku cholinga chake chonse cha utumiki wake pa dziko lapansi, kukonza anthu kupyolera mu vumbulutso la Mulungu. Mwa Khristu adavekedwa pamaso pa anthu chisomo cha tate ndi  ungwiro wosayerekezeka wa Atate. Mu pemphero lake Iye asanapachikidwe, Iye analengeza, “Ine ndaliwonetsera dzina lanu.” “Ine ndakulemekezani pa dziko lapansi; Ine ndatsiriza ntchito imene munandipatsa Ine ndichite.” Pamene cholinga cha utumiki wake chinali chitakwaniritsidwa, ndicho chivumbulutso cha Mulungu ku dziko lapansi, —Mwana wa Mulungu analengeza kuti ntchito yake inakwaniritsidwa, ndikuti khalidwe la Atate linawonetseredwa kwa anthu. {Signs of the Times, January 20, 1890, par. 9}