tatewachikondi.com
Wolemba Adrian Ebens
Losindikizidwa Januware 28, 2021
Zokopera 577

Zitsanzo za dziko lonse za moyo zonse zimatizungulira ife. Zonse zimachokera ku Chitsanzo Chaumulungu choyambirira chotsika kuchokera kwa Atate, kudzera mwa Mwana ndipo chimapezeka pa mulingo uliwonse wa moyo.

Dzuwa ndi mwezi, mbewu ndi chomera, kholo ndi mwana, mfumu ndi dziko, Chipangano Chakale – Chipangano Chatsopano, Chitsanzo cha Gwero ndi Njira ndiye nfungulo.

Njira yowukira, yotsutsa yalowa miyoyo ya abambo, ndi amai, ndi mitima ndi malingaliro a olamulira ndi atsogoleri. Onse ayenera kusankha chitsanzo chawo cha moyo kapena imfa. Malemba opatulika amatilimbikitsa ife kusankha.